MSOGOLERI WA DZIKOLI HAKAINDE HICHILEMA WATI AZAIMABE NJI POKWIMITSA MALAMULO OLETSA KUBA MANKHWALA ADZIKOLI
July 15,2025
Msogoleri wa dzikoli olemekezeka Hakainde Hichilema walengeza kuti boma lizakwimitsa malamulo ndicolinga cofuna kuthetsa mcitidwe wakuba mankhwala mzipatala za boma.
Msogoleri Hichilema wati sazakhalira kumbuyo aliyense yemwe adzapezeka kuti anazembetsa mankhwala omwe anayenera kuthandiza anthu.
Iye wati izi nkulingana ndi zomwe kabungwe ka kafukufuku ka Pricewatercoopers (PWC) kalengeza komwe boma linakhazikitsa kukaunguza za umbava wa mankhwala.
Nkulingana ndi zomwe walemba olumikiza uthenga wa ku nyumba ya statehouse Clayson Hamasaka yemwe walemba kuti Kabungwe ka PWC kapeza kuti nkhani yozembetsa mankhwala ndi zinthu zina zokhuza za umoyo zinaculukirapo komanso KuKwezeka kwa mitengo kwa zinthu zina zokhuza umoyo.
Izi ndi zina zomwe zinapangitsa Dziko la USA kuimitsa ma thandizo okwanira pa 50 million Ndalama ya America.
Msogoleri Hichilema wati boma lakhazikitsa kale kabungwe komwe kazakhwimitsa malamulo ndicolinga cofuna kulongosola kayendetsedwe ka mankhwala adzikoli.
©️Cyclone News

