MTSOGOLERI WADZIKOLI WAKHUZIDWA NDI IMFA YA BAMBO SIKOTA WINA.

By James sakala.

Mtsogoleri wa dzikoli olemekezeka Hakainde Hichilema wati ndi okhudzidwa ndi kumwalira Kwa bambo Sikota Wina.

Msogoleri wati bambo wina anali m’modzi mwa anthu omwe anamenyera ufulu kuti tikhalenao mtendere nthawi ino.

Mopitiliza iye wati nchito yabwino ya malemu Wina yomenyera ufulu wa dzikoli siingabisike komanso ndiyosaiwalika.

Sikota Wina wamwalira ndi zaka makumi asanu ndi anai (90) Mu chipatala capamwamba camaphunziro a sukulu la ukachenjede la University Teaching Hospital (UTH) Lero laliwitsiri.

Bambo Wina anagwira nchito m’maudindo osiyana siyana monga nduna ya Zaumoyo ,zokopa alendo ,zamaboma ang’ono ang’ono ndi maudindo ena ambiri.

Tingoti mzimu wao uutse mumtendere.

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here