MSOGOLERI WA NIGERIA WALANDIRA THUPI LA MSOGOLERI WA KALE OLEMEKEZEKA MUHAMMADU BUHARI
July 15,2025
Msogoleri wa Dziko la Nigerian Bola Tinubu lero walandira thupi la Malemu Muhammadu Buhari pa bwalo la ndege la Umaru Musa Yar’Adua international Airport mu boma la Katsina.
Ndege yonyamula mtembo wa Malemu Muhammadu inatera pa bwalolo la ndege ndi nthawi ya 2 koloko madzulo.
Msogoleri Muhammadu wamwalira pa Sabata , July 13,2025 mdziko la London ku Chipatala cochedwa London Hospital.
Thupi la Msogoleri Muhammadu lapatsidwa Mwambo wa atsogoleri pa bwalo la ndege akalibe kupita nalo ku malo osungira mitembo.
©️ UPND MEDIA TEAM

