HAKAINDE HICHILEMA ALANKULA NDI NYUMBA YA MALAMULO YA DZIKO LA EUROPE.

23/06/2022

Mtsogoleri wadzikoli olemekezeka Bambo Hakainde Hichilema walankhula mumsonkhano wa nduna za nyumba ya malamulo La mgwirizano wa maiko a Europe womwe wacitikira mum’mzinda wa Brussels mdziko la Belgium.

Mtsogoleri Hakainde wabvumbulutsa mfundo zikulu zikulu maka zokhuza kunkhani ya Bata ndi mtendere komanso zitukuko zosiyana siyana za dzikoli.

Mopitiliza iye wayamikira mgwirizano womwe ulipo pakati pa dziko lathu ndi maiko amgwirizano aku Europe.

KUMBALI YA ZAUFULU NDI ZIPHUPHU

mtsogoleri wathu wafuula ndikunena kuti dziko lomwe iye anapeza pomwe analowa pa utsogoleri linali loonongeka komanso lodzala ndi anthu ozikonda maka kumbali ya zacuma komanso ku ziphuphu.

Mopitiliza wati zocitika zambiri muboma lapita zinali zokomera anthu ocepa cabe koma kupatsa cilango anthu ambiri-mbiri adziko la Zambia.

Iye wati munalibe mtendere monga ufulu olankhula ,kapena kutengako mbali kuzinthu zobweretsa zitukuko.

Ndipo iye wanenetsa kuti palipano ufulu komanso kulondola lamulo zikubwezedwanso mdziko la Zambia.
Mtsogoleri wathu wasimba Niti iye akunyadira mbiri yabwino yomwe ikumveka ndi dzikoli tsopano.

Ndipo iye walongeza kuti ndi boma lake mabungwe odziimira paokha adzakala aufulu kutengako mbali mkayendetsedwe kadzikoli.

KUMBALI YA MALAMULO
Mtsogoleri Hakainde wati akuika amalamulo abwino m’malo mwake omwe azalongosola kayendetsedwe ka dzikoli.

KUMBALI YA ANYAMATA NDI ATSIKANA.

Mtsogoleri wathu wabvumbulutsa kuti akutenga kupambana masankho ngati ngati njira yo onetsetsa kuti Zambia Ali ndi tsogolo labwino lokomera anyamata ndi atsikana.

Mopitiliza wati ati iye akulaka laka kupanga dzikolathu kukhala lozama pa kafukufuku wa zitukuko zamakono kupyolera mu anyamata ndi atsikana.

Ndipo watsimikidzanso kuti ndi anyamata ndi atsikana omwe akukonzeranso dziko lathu ndi cifukwa cace anaika maphunziro aulele zomwe zapangitsa kuti ana ambiri ocokera mumabanja obvutika apeze mpata wa maphunziro.

Mopitiliza mtsogoleri Hakainde wati boma laika padera ndalama zambiri mbiri kupyolera mu Ndalama zam’madera zetchedwa CDF kuti zithandi zire zinchito zotukuka dzikoli kupitira mu nyamata ndi atsikana akumaderako.

MBALI YA ZACUMA KOMANSO MGWIRIZANO WA ZAMBIA NDI EUROPE.

Mtsogoleri wathu bambo Hakainde Hichilema wati Zambia sanacite bwino kumbali ya zacuma zaka khumi zapitazo ndipo izi zanapangitsa umoyo wa anthu kubvutika cifukwa ca kukwera mitengo Kwa zinthu monga zakudya ndi nkhani ya mayendedwe.

Iye wati izi zatere cingakhale Zambia Ali odalitsika ndi cuma cambiri monga miyala ya mkuwa ndi golide ,madzi ndi nthaka yabwino ya ulimi.

Iye wati zimenezi sizinayenera kutero.

Mtsogoleri wati kukonzaso dzikoli kumbali ya zacuma ndiye colinga ca boma latsopanoli.

Iye wati akuyembekezera kuti mgwirizano wa Zambia ndi maiko a Europe uzathandizira kuika Zambia m’malo mwake kumbali ya zacuma.

Iye wati nchifukwa cake Zambia akutsegula njira kwa onse ocita malonda.

KUMBALI YA ZAKUDYA NDI KUSINTHA KWA NYENGO.

Mtsogoleri wafotokoza kuti monga dziko lapansi komanso Afrika likupita mumasauso akucepekera Kwa zakudya ,Zambia ndi olimilira nji ,ndipo Ali okonzeka kukhala ndi zakudya zambiri.

Bambo Hichilema wati mgwilizano pakati pa Zambia ndi Europe mnkhani ya zaulimi zingapangitse Zambia kupambana ndithu.

Izi ndi Zina cabe mwa mfundo zikulu zikulu zomwe mtsogoleri Hakainde Hichilema wabvumbulutsa kuja kumsonkhano wa nduna za nyumba ya malamulo la dziko la Europe.

(C) THE FALCON

287763317_620333092782755_4883240900812156821_n
287781691_620333046116093_6767084082700866946_n
287743628_620332676116130_8631069994110599898_n
288916544_620332729449458_1484329701428103009_n
289057258_620333356116062_6728501617132600819_n
289005556_620332789449452_4072509692997543478_n
289357761_620333209449410_5129363478623995045_n
289175480_620333402782724_5321963815661688698_n
289379709_620333492782715_6268672023579654653_n
393613

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here